Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu.
Genesis 34:22 - Buku Lopatulika Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komatu anthu ameneŵa adzavomera kukhala pakati pathu ndi kusakanizana nafe, kuti tikhale mtundu umodzi, pokhapokha ifeyo tikaumbala amuna onse monga amachitira iwowo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komatu anthuwa adzavomereza kukhala amodzi a ife pokhapokha ngati amuna onse pakati pathu atachita mdulidwe monga alili iwo. |
Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu.
Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m'dzikomo, achite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao aakazi akhale aakazi athu, tiwapatse amenewa ana athu aakazi.
Kodi ng'ombe zao ndi chuma chao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tivomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.