Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye.
Genesis 34:18 - Buku Lopatulika Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wake wa Hamori. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wake wa Hamori. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mau ameneŵa adakondweretsa kwambiri Hamori ndi mwana wake Sekemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mawu amenewa anakondweretsa Hamori ndi mwana wake Sekemu. |
Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye.
Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wake.
Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake.