Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani.
Genesis 34:16 - Buku Lopatulika pamenepo tidzakupatsani inu ana athu aakazi, ndipo tidzadzitengera ana anu aakazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pamenepo tidzakupatsani inu ana athu akazi, ndipo tidzadzitengera ana anu akazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo tidzakulolani kuti mukwatire ana athu, ndipo ifenso tidzakwatira ana anu. Tsono tidzakhazikika pakati panu ndi kusanduka fuko limodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka tidzakulolani kuti mukwatire ana athu, ifenso tizikwatira ana anu. Choncho tidzakhala pakati panu ndipo tidzakhala anthu amodzi. |
Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani.
Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye.