Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.
Genesis 34:13 - Buku Lopatulika Ndipo ana ake aamuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana ake amuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ana a Yakobe adayankha Sekemu ndi bambo wake Hamori moŵanyenga, popeza kuti Sekemu adaamchititsa manyazi Dina mlongo wao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana a Yakobo anayankha Sekemu ndi abambo ake, Hamori mwachinyengo chifukwa mlongo wawo, Dina anali atayipitsidwa. |
Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.
nati kwa iwo, Sitingathe kuchita ichi, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; chifukwa kumeneko ndiko kutichepetsa ife.
Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.
ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima.
Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.
nati, Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo.
Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.
Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.
Koma Samisoni, ananena nao, Nthawi ino ndikhala wosapalamula pa Afilisti, powachitira choipa ine.