Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 34:12 - Buku Lopatulika

Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tandiwuzani mphatso imene mufuna, ndipo mutchule mtengo uliwonse wolowolera. Ine ndidzakupatsani zonse zimene mungatchule, malinga mukandilola kumkwatira mkaziyu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tchulani mtengo wamalowolo umene ndiyenera kupereka, ndipo ndipereka. Ndidzakupatsani chilichonse chimene mukufuna malingana inu mukandipatsa namwaliyu kuti ndimukwatire.”

Onani mutuwo



Genesis 34:12
13 Mawu Ofanana  

Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zagolide, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake.


Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele mwana wanu wamkazi wamng'ono.


Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.


Ndipo Sekemu anati kwa atate wake wa mkazi ndi kwa abale ake, Tipeze ufulu pamaso panu, chimene mudzanena kwa ine ndidzapereka.


Ndipo ana ake aamuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao,


Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Saulo, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi.


Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake.


M'mwemo ndinadzigulira iye ndi masekeli khumi ndi asanu a siliva, ndi homeri ndi leteki wa barele;


Koma iwo ananena kwa Iye, Ife tilibe kanthu pano koma mikate isanu, ndi nsomba ziwiri.


Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.