Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 34:1 - Buku Lopatulika

Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsiku lina Dina mwana wa Yakobe wobadwa kwa Leya, adapita kukacheza ndi akazi ena am'dzikomo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsopano Dina, mwana amene Leya anaberekera Yakobo, anapita kukacheza ndi akazi ena a mʼdzikolo.

Onani mutuwo



Genesis 34:1
10 Mawu Ofanana  

Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Muhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Eloni Muhiti.


Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?


Ndipo anaona Esau kuti Isaki anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko; ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani;


Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana aakazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere.


Pambuyo pake ndipo anabala mwana wamkazi, namutcha dzina lake Dina.


Ndipo anamanga pamenepo guwa la nsembe, natcha pamenepo El-Elohe-Israele.


Amenewo ndi ana aamuna a Leya, amene anambalira Yakobo ku Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.


Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? Udzachitanso manyazi ndi Ejipito monga unachita manyazi ndi Asiriya.


Ndipo aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.


akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.