Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.
Genesis 33:6 - Buku Lopatulika Ndipo adzakazi anayandikira ndi ana ao, nawerama pansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo adzakazi anayandikira ndi ana ao, nawerama pansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adzakazi aja adadza pamodzi ndi ana ao, nagwada pansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono antchito aja anayandikira naweramitsa mitu pansi. |
Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.
Ndiponso Leya ndi ana ake anayandikira nawerama pansi: pambuyo pake anayandikira Yosefe ndi Rakele, nawerama pansi.