Ndipo Labani anali ndi ana aakazi awiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele.
Genesis 33:2 - Buku Lopatulika Ndipo anaika adzakazi ndi ana ao patsogolo, ndi Leya ndi ana ake pambuyo pao, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaika adzakazi ndi ana ao patsogolo, ndi Leya ndi ana ake pambuyo pao, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adatsogoza adzakaziwo pamodzi ndi ana ao. Leya ndi ana ake ankatsata pambuyo pao, Rakele ndi Yosefe ankadza pambuyo penipeni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anayika antchito ndi ana awo patsogolo, kenaka nʼkubwera Leya ndi ana ake, ndipo pambuyo pawo Rakele ndi Yosefe. |
Ndipo Labani anali ndi ana aakazi awiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele.
Ndipo Yakobo analowanso kwa Rakele, namkondanso Rakele kopambana Leya, namtumikira Labani zaka zisanu ndi ziwiri zinanso.
Ndipo Yakobo anatukula maso ake, taonani, anadza Esau, ndi pamodzi naye anthu mazana anai. Ndipo anagawira ana kwa Leya, ndi kwa Rakele, ndi kwa adzakazi awiri aja.
Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkulu wake.
Koma Israele anamkonda Yosefe koposa ana ake onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wake; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro.
amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, chipululu, dziko louma, bwinja.
Ndipo adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira.