Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, kudera la ku Edomu.
Genesis 33:16 - Buku Lopatulika Ndipo Esau anabwerera tsiku lomwelo kunka ku Seiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Esau anabwera tsiku lomwelo kunka ku Seiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero pa tsiku limenelo Esau adanyamuka ulendo kubwerera ku Seiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho tsiku limenelo Esau anayamba ulendo wobwerera ku Seiri. |
Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, kudera la ku Edomu.
Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga.
Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti.
Ndipo akalonga a Afilisti anamkwerera mkaziyo, nanena naye, Umkope nuone umo muchokera mphamvu yake yaikulu, ndi umo tingakhoze kumtha khama, kuti timmange kumzunza; ndipo tidzakupatsa aliyense ndalama mazana khumi ndi limodzi.