Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, navutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamira, zikhale makamu awiri;
Genesis 32:8 - Buku Lopatulika ndipo anati, Akafika Esau pa khamu limodzi nalikantha, linalo lotsala lidzapulumuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anati, Akafika Esau pa khamu limodzi nalikantha, linalo lotsala lidzapulumuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Esau akabwera, ndipo akachita nkhondo ndi gulu loyambali, gulu linalo lingathe kuthaŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mʼmaganizo ake iye ankanena kuti, “Ngati Esau atabwera ndi kuthira nkhondo gulu limodzi, gulu lina lotsalalo likhoza kupulumuka.” |
Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, navutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamira, zikhale makamu awiri;
Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isaki, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino:
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.