Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 32:32 - Buku Lopatulika

Chifukwa chake ana a Israele samadya mtsempha ya thako ili pa nsukunyu ya ntchafu kufikira lero: chifukwa anakhudza nsukunyu ya ntchafu ya Yakobo pa mtsempha ya thako.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa chake ana a Israele samadya mtsempha ya thako ili pa nsukunyu ya ntchafu kufikira lero: chifukwa anakhudza nsukunyu ya ntchafu ya Yakobo pa mtsempha ya thako.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nchifukwa chake mpaka lero lino zidzukulu zonse za Israele sizidya nyama yapanyung'unyu, chifukwa ndi pa mtsempha wa panyung'unyu pomwe Yakobe adaamenyedwa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nʼchifukwa chake mpaka lero Aisraeli sadya nyama ya pa nyungʼunyu chifukwa Yakobo anakhudzidwa pa nyungʼunyu.

Onani mutuwo



Genesis 32:32
6 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene anaona kuti sanamgonjetse, anakhudza nsukunyu ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye.


Ndipo kudamchera iye pamene anaoloka pa Penuwele, ndipo iye anatsimphina ndi ntchafu yake.


Ndipo Yakobo anatukula maso ake, taonani, anadza Esau, ndi pamodzi naye anthu mazana anai. Ndipo anagawira ana kwa Leya, ndi kwa Rakele, ndi kwa adzakazi awiri aja.


Ndipo Yerobowamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efuremu, nakhalamo, natulukamo, namanga Penuwele.


Ndipo anachokapo kukwera ku Penuwele, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penuwele anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.


Chifukwa chake angakhale ansembe, angakhale ena akulowa m'nyumba ya Dagoni, palibe woponda pa chiundo cha Dagoni ku Asidodi, kufikira lero lino.