Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamutcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara.
Genesis 32:28 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu uja adati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobe. Walimbana ndi Mulungu ndi anthu, ndipo wapambana. Motero dzina lako lidzakhala Israele.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo munthuyo anati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobo koma Israeli, chifukwa walimbana ndi Mulungu ndi anthu ndipo wapambana.” |
Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamutcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara.
Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.
Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.
Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo.
Ndipo Mulungu anati kwa iye, Dzina lako ndi Yakobo; dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma dzina lako lidzakhala Israele: ndipo anamutcha dzina lake Israele.
natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova.
Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ziwerengo cha mafuko ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israele.
Mpaka lero lino achita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sachita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena chilamulo, kapena choikika adachilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamutcha Israele,
Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga.
Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;
Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.
Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).
Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.
Pomwepo Saulo anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzachita ndithu champhamvu, nudzapambana. Chomwecho Davide anamuka, ndipo Saulo anabwera kwao.