Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kuchita kanthu usadafike kumeneko. Chifukwa chake anatcha dzina la mzindawo Zowari.
Genesis 32:25 - Buku Lopatulika Ndipo pamene anaona kuti sanamgonjetse, anakhudza nsukunyu ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene anaona kuti sanamgonjetsa, anakhudza nsukunyu ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthuyo ataona kuti sakuphulapo kanthu, adamenya Yakobe m'nyung'unyu, nyung'unyuyo nkuguluka polimbanapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene munthuyo anaona kuti sangathe kumugonjetsa, anakhudza nyungʼunyu ya pa ntchafu ya Yakobo ndipo inaguluka polimbanapo. |
Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kuchita kanthu usadafike kumeneko. Chifukwa chake anatcha dzina la mzindawo Zowari.
Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
Chifukwa chake ana a Israele samadya mtsempha ya thako ili pa nsukunyu ya ntchafu kufikira lero: chifukwa anakhudza nsukunyu ya ntchafu ya Yakobo pa mtsempha ya thako.
Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.
Atero Yehova Woyera wa Israele ndi Mlengi wake, Ndifunse Ine za zinthu zimene zilinkudza; za ana anga aamuna, ndi za ntchito ya manja anga, ndilamulireni Ine.
Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.