Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse ine mkazi wanga, chifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.
Genesis 32:22 - Buku Lopatulika Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ake awiri, ndi adzakazi ake awiri, ndi ana ake aamuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa dooko la Yaboki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ake awiri, ndi adzakazi ake awiri, ndi ana ake amuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa dooko la Yaboki. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Usiku womwewo Yakobe adadzuka natenga akazi ake aŵiri, ndi adzakazi ake aŵiri aja, pamodzi ndi ana ake khumi ndi mmodzi, naoloka mtsinje wa Yaboki padooko pake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usiku umenewo Yakobo anauka natenga akazi ake awiri, antchito ake awiri ndi ana ake aamuna khumi ndi mmodzi nawoloka pa dooko la mtsinje wa Yaboki. |
Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse ine mkazi wanga, chifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.
Momwemo naolotsa mphatso patsogolo pake: ndipo iye yekha anagona usiku womwewo pachigono.
Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamutcha dzina lake Benoni; koma atate wake anamutcha Benjamini.
Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikize; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi mizinda ya kumapiri, ndi kwina kulikonse Yehova Mulungu wathu anatiletsa.
Koma ndinapatsa Arubeni ndi Agadi kuyambira ku Giliyadi kufikira ku mtsinje wa Arinoni, pakati pa chigwa ndi malire ake, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.
Sihoni mfumu ya Aamori wokhala mu Hesiboni, wochita ufumu kuyambira ku Aroere ndiwo m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi pakati pa chigwa ndi pa Giliyadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;
Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Chifukwa Israele analanda dziko langa pakukwera iye kuchokera ku Ejipito, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordani; ndipo tsopano undibwezere maikowa mwamtendere.