Pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu.
Genesis 32:19 - Buku Lopatulika Ndipo anauzanso wachiwiri ndi wachitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau chotero, pamene mukomana naye: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anauzanso wachiwiri ndi wachitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau chotero, pamene mukomana naye: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adauzanso mnyamata wake wachiŵiri mau omwewo, ndi wachitatu, mpaka onse amene ankayenda motsogoza zoŵeta. Adaŵauza kuti, “Zimenezi ndizo mukauze Esau, mukakumana naye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anawuza mawu omwewo kwa wachiwiri, wachitatu ndi ena onse amene ankayenda motsogoza ziwetozo kuti, “Inunso munene zomwezo kwa Esau mukakumana naye. |
Pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu.
ndiponso muziti, Ndiponso, taonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu. Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pake ndidzaona nkhope yake; kapena adzandilandira ine.
Nati kwa anyamata ake, Nditsogolereni; onani ndidza m'mbuyo mwanu. Koma sanauze mwamuna wake Nabala.