Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkulu wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? Za yani zimenezi patsogolo pako?
Genesis 32:18 - Buku Lopatulika Pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwe ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za mtumiki wanu Yakobe, ndipo akuzitumiza kwa inu mbuyake, kuti zikhale mphatso. Yakobe mwiniwake ali m'mbuyo mwathumu.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za wantchito wanu, Yakobo, ndipo wazipereka kwa inu, Esau, mbuye wake ngati mphatso. Mtumiki wanuyu akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” |
Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkulu wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? Za yani zimenezi patsogolo pako?
Ndipo anauzanso wachiwiri ndi wachitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau chotero, pamene mukomana naye: