Ndipo anazipereka zimenezo m'manja a anyamata ake, gulu pa lokha gulu pa lokha: ndipo anati kwa anyamata ake, Taolokani patsogolo panga, tachitani danga pakati pa magulu, lina ndi lina.
Genesis 32:17 - Buku Lopatulika Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkulu wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? Za yani zimenezi patsogolo pako? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkulu wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? Za yani zimenezi patsogolo pako? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adauza mnyamata woyamba kuti, “Mbale wanga Esau akakumana nawe ndi kukufunsa kuti, ‘Kodi mbuyako ndani? Nanga ukupita kuti? Nanga zoŵeta zili patsogolo pakozi nza yani?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anawuza mnyamata wa gulu loyamba kuti, “Ngati ukumana naye mʼbale wanga Esau nakufunsa kuti, ‘Ndinu antchito a yani, ndipo mukupita kuti? Nanga ziweto zonse zili patsogolo pakozi ndi za yani?’ |
Ndipo anazipereka zimenezo m'manja a anyamata ake, gulu pa lokha gulu pa lokha: ndipo anati kwa anyamata ake, Taolokani patsogolo panga, tachitani danga pakati pa magulu, lina ndi lina.
Pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu.
Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkulu wake.