Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.
Genesis 32:11 - Buku Lopatulika Mundipulumutsetu ine m'dzanja la mkulu wanga, m'dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundipulumutsetu ine m'dzanja la mkulu wanga, m'dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndapota nanu, pulumutseni ku mphamvu za mbale wanga Esau. Ndikuwopa kuti mwina akubwera kudzatithira nkhondo, ndipo tonsefe adzatiwononga pamodzi ndi akazi ndi ana omweŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipulumutseni mʼdzanja la mʼbale wanga Esau, popeza ndikuopa kuti mwina akubwera kudzandithira nkhondo pamodzi ndi akazi ndi ana omwe. |
Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.
Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.
Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wake wamkulu: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wake wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkulu wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wake kuti adzakupha iwe.
Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, kudera la ku Edomu.
Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, navutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamira, zikhale makamu awiri;
Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo.
Pomwepo Davide mfumu analowa, nakhala pansi pamaso pa Yehova; nati, Ine ndine yani, Yehova Mulungu, ndi banja langa ndi chiyani kuti munandifikitsa pano?
Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri; ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andipambana.
Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.
Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.
Kupembedza mbale utamchimwira nkovuta, kulanda mzinda wolimba nkosavuta; makangano akunga mipiringidzo ya linga.
Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.
Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribele; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ake.
Mukachipeza chisa cha mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi make alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga make pamodzi ndi ana;
Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinachimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira Abaala ndi Asitaroti, koma mutipulumutse tsopano m'manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu.
Chifukwa chake Yehova akhale woweruza, naweruze pakati pa ine ndi inu, nayang'anire, nandigwirire moyo, nandipulumutse m'dzanja lanu.