Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathothomathotho ndi zamawangamawanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamawangamawanga ndi zamathothomathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.
Genesis 31:8 - Buku Lopatulika Akati chotero, Zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako, zoweta zonse zinabala zamathothomathotho; ndipo akati iye chotere, Zamipyololomipyololo zidzakhala malipiro ako, ziweto zonse zinabala mipyololomipyololo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akati chotero, Zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako, zoweta zonse zinabala zamathothomathotho; ndipo akati iye chotere, Zamipyololomipyololo zidzakhala malipiro ako, ziweto zonse zinabala mipyololomipyololo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi zonse Labani akanena kuti, ‘Zoŵeta zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako,’ zoŵeta zonse zinkakhala zamathothomathotho. Ndipo akanena kuti, ‘Zamipyololo zikhala malipiro ako,’ zoŵeta zonse zinkangokhala zamipyololo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene abambo anu anati, ‘Zamawangamawanga zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana amawangamawanga; ndipo pamene anati, ‘Zamichocholozi zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana a michocholozi. |
Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathothomathotho ndi zamawangamawanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamawangamawanga ndi zamathothomathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.
Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathothomathotho, ndi zamawangamawanga.