Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe.
Genesis 31:6 - Buku Lopatulika Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nonse aŵirinu mukudziŵa bwino kuti ndidagwira ntchito kwa bambo wanu ndi mphamvu zanga zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mukudziwa kuti ndagwirira ntchito abambo anu ndi mphamvu zanga zonse, |
Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe.
Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe chomwe ndakutumikira iwe ndi chomwe zachita zoweta zako ndi ine.
Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa.
Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali.