Ndipo Labani anali ndi ana aakazi awiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele.
Genesis 31:4 - Buku Lopatulika Ndipo Yakobo anatumiza naitana Rakele ndi Leya adze kubusa ku zoweta zake, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yakobo anatumiza naitana Rakele ndi Leya adze kubusa ku zoweta zake, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yakobe adatumiza mau kwa Rakele ndi kwa Leya kuti akakumane naye kubusa kumene kunali zoŵeta zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Yakobo anatumiza mawu kukayitana Rakele ndi Leya kuti abwere ku busa kumene ankaweta ziweto zake. |
Ndipo Labani anali ndi ana aakazi awiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele.
Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe.
ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekere ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.