Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'michera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.
Genesis 30:41 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m'micheramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m'micheramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoŵeta zamphamvu zikamakwerewa, Yakobe ankazikhazikira nthambi zija kumaso kwake pa malo omwera, kuti pakutero zitenge maŵere pafupi ndi nthambizo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yakobo ankayika nthambi zija momwera madzi pamene ziweto zamphamvu zazikazi zinkakweredwa pofuna kuti zitenge mawere pakumwa madzi moyangʼanana ndi nthambi zija. |
Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'michera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.
Ndipo Yakobo analekanitsa anaankhosa naziika pa zoweta za kuti ziyang'anire zamipyololomipyololo, ndi zakuda zonse za m'zoweta za Labani.
Koma pamene ziweto zinali zofooka, sanaziike zimenezo: ndipo zofooka, zinali za Labani, ndi zolimba zinali za Yakobo.