Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathothomathotho, ndi zamawangamawanga.
Genesis 30:40 - Buku Lopatulika Ndipo Yakobo analekanitsa anaankhosa naziika pa zoweta za kuti ziyang'anire zamipyololomipyololo, ndi zakuda zonse za m'zoweta za Labani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yakobo analekanitsa anaankhosa naziika pa zoweta za kuti ziyang'anire zamipyololomipyololo, ndi zakuda zonse za m'zoweta za Labani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yakobe adaika anaankhosa padera, naika nkhosa zina kuti ziyang'anane ndi zoŵeta za Labani zamathothomathotho ndi zakuda. Mwa njira imeneyi adapeza zoŵeta zakezake, ndipo sadazisokoneze ndi zoŵeta za Labani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yakobo anayika padera ana a ziweto zija. Koma ziweto zina anaziyika kuti ziyangʼanane ndi za Labani, zimene zinali za mawangamawanga ndi zakuda. Motero anapeza ziweto zakezake, ndipo sanazisakanize ndi za Labani. |
Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathothomathotho, ndi zamawangamawanga.
Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m'micheramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo.