Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe chomwe ndakutumikira iwe ndi chomwe zachita zoweta zako ndi ine.
Genesis 30:30 - Buku Lopatulika Chifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zachuluka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kulikonse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zachuluka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kulikonse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kale munali ndi zoŵeta pang'ono koma tsopano zachuluka, ndipo Chauta wakudalitsani chifukwa cha ine. Tsopano ndiyenera kusamala banja langa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Poyamba munali nazo zochepa ine ndisanabwere, koma tsopano zachuluka. Yehova wakudalitsani chifukwa cha ine. Ndi nthawi tsopano kuti nane ndisamalire banja langa.” |
Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe chomwe ndakutumikira iwe ndi chomwe zachita zoweta zako ndi ine.
Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandichitira ine chotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako.
Munthuyo ndipo analemera kwambiri, nali nazo zoweta zambiri, ndi akapolo aamuna ndi aakazi, ndi ngamira, ndi abulu.
Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana.
Pakuti dziko limene munkako kulilandira ndi losanga dziko la Ejipito lija mudatulukako, kumene kuja munafesa mbeu zanu, ndi kuzithirira ndi phazi lanu, monga munda watherere;
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.