Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma.
Genesis 30:23 - Buku Lopatulika Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wachotsa manyazi anga; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wachotsa manyazi anga; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyenso adatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna. Ndipo adati, “Mulungu wandichotsa manyazi a uchumba wanga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Rakele anatenga pathupi nabala mwana wamwamuna ndipo anati, “Mulungu wandichotsera manyazi anga.” |
Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma.
Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya chakudya chathuchathu ndi kuvala zovala zathuzathu; koma titchedwe dzina lako; chotsa chitonzo chathu.
Ambuye wandichitira chotero m'masiku omwe Iye anandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.
kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria.
Ndipo anati kwa atate wake, Andichitire ichi, andileke miyezi iwiri, kuti ndichoke ndi kutsikira kumapiri, ndi kulirira unamwali wanga, ine ndi anzanga.