Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana aamuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni.
Genesis 30:21 - Buku Lopatulika Pambuyo pake ndipo anabala mwana wamkazi, namutcha dzina lake Dina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pambuyo pake ndipo anabala mwana wamkazi, namutcha dzina lake Dina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake adabala mwana wamkazi, namutcha Dina. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patapita nthawi Leya anabereka mwana wamkazi ndipo anamutcha Dina. |
Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana aamuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni.
Ndipo Mulungu anakumbukira Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m'mimba mwake.
Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wake ndi lupanga, natulutsa Dina m'nyumba ya Sekemu nachoka naye.
Amenewo ndi ana aamuna a Leya, amene anambalira Yakobo ku Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.