Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m'thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.
Genesis 30:16 - Buku Lopatulika Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Yakobe ankabwera madzulo kuchokera ku munda, Leya adatuluka kukamlonjera, nati “Lero mugone kunyumba kwanga kuno, chifukwa cha mankhwala a chisulo ondifunira mwana wanga.” Motero Yakobe adakhala ndi Leya usiku umenewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho pamene Yakobo ankabwera kuchokera ku munda madzulo, Leya anapita kukakumana naye nati, “Lero mukagona ku nyumba chifukwa ndakubwerekani ndi mankhwala wobereketsa a mwana wanga.” Choncho usiku umenewo Yakobo anakalowa kwa Leya. |
Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m'thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.
Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.
Ndipo Mulungu anamvera Leya, ndipo anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu.