Genesis 30:13 - Buku Lopatulika Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana aakazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana akazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Leya adati, “Ndakondwa! Ndipo akazi adzanditchula wamwai.” Motero mwanayo adamutcha Asere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Leya anati, “Ndakondwa bwanji! Amayi adzanditcha ine wokondwa.” Choncho anamutcha Aseri. |
ndipo ana aamuna a Zilipa mdzakazi wake wa Leya: ndiwo Gadi ndi Asere: amenewo ndi ana aamuna a Yakobo amene anabala iye mu Padanaramu.
Ndi ana aamuna a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele.
Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi; ndiye wobadwa yekha wa amake; ndiye wosankhika wa wombala. Ana aakazi anamuona, namutcha wodala; ngakhale akazi aakulu a mfumu, ndi akazi aang'ono namtamanda.
chifukwa Iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wake; pakuti taonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala.