Genesis 30:11 - Buku Lopatulika Ndipo Leya anati, Wamwai ine! Ndipo anamutcha dzina lake Gadi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Leya anati, Wamwai ine! Ndipo anamutcha dzina lake Gadi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Leya adati, “Ndachita mwai.” Motero mwanayo adamutcha Gadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Leya anati, “Mwayi wangawo!” Choncho anamutcha Gadi. |
ndipo ana aamuna a Zilipa mdzakazi wake wa Leya: ndiwo Gadi ndi Asere: amenewo ndi ana aamuna a Yakobo amene anabala iye mu Padanaramu.
Ndi ana aamuna a Gadi: Zifiyoni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Eziboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli.
Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mulungu wamwai gome, ndi kudzazira mulungu waimfa zikho za vinyo wosakaniza;
A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;