Genesis 30:10 - Buku Lopatulika Ndipo Zilipa mdzakazi wake wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Zilipa mdzakazi wake wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Zilipa adabala mwana wamwamuna. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zilipa, wantchito wa Leya, anaberekera Yakobo mwana wamwamuna. |
Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wake, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.
ndipo ana aamuna a Zilipa mdzakazi wake wa Leya: ndiwo Gadi ndi Asere: amenewo ndi ana aamuna a Yakobo amene anabala iye mu Padanaramu.
Ndi kumalire a Zebuloni, kuyambira kumbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Gadi, limodzi.
A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.