Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 3:21 - Buku Lopatulika

Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wake malaya azikopa, nawaveka iwo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wake malaya azikopa, nawaveka iwo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo Chauta adasokera Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa naŵaveka onse aŵiriwo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa ndipo anawaveka.

Onani mutuwo



Genesis 3:21
8 Mawu Ofanana  

Ndipo mwamuna anamutcha dzina la mkazi wake, Heva; chifukwa ndiye amake wa amoyo onse.


Ndipo anati Yehova Mulungu, Taonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziwa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse,


Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana;


ndipo zimene tiziyesa zochepa ulemu m'thupi, pa izi tiika ulemu wochuluka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala nacho chokometsera choposa.


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.