Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.
Genesis 29:9 - Buku Lopatulika Ali chilankhulire nao, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wake, chifukwa anaziweta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ali chilankhulire nao, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wake, chifukwa anaziweta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yakobe akulankhulabe ndi iwowo, Rakele adafika ndi nkhosa za atate ake. Iyeyo ndiye ankaŵeta nkhosazo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ali chiyankhulire nawo, Rakele anafika ndi nkhosa za abambo ake popeza ndiye amene ankaweta nkhosazo. |
Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.
Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wake wa amake, ndi nkhosa za Labani mlongo wake wa amake, Yakobo anayandikira nagubuduza kuuchotsa mwala pachitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wake wa amake.
Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa.
Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora.
Pakukwera kumzindako anapeza anthu aakazi alikutuluka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?