Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake.
Genesis 29:8 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo aja adayankha kuti, “Sitingathe kutero mpaka nkhosa zonse zitasonkhana pamodzi, ndipo mwala wa pamwamba pa chitsimewo titaukunkhuniza. Apo tingathe kuzipatsa madzi nkhosazo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anayankha, “Ayi sitingatero. Tidikira mpaka nkhosa zonse zisonkhane. Zikatero, tigubuduza mwalawu kuwuchotsa pamwamba pa chitsimepo, kenaka nʼkuzimwetsa madzi nkhosazo.” |
Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake.
Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni.
nati kwa iwo, Sitingathe kuchita ichi, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; chifukwa kumeneko ndiko kutichepetsa ife.
Ndipo anamuikira iye chake pa yekha, ndi iwo chao pa okha, ndi Aejipito akudya naye chao pa okha; chifukwa Aejipito sanathei kudya chakudya pamodzi ndi Ahebri: chifukwa kuchita chomwecho nkunyansira Aejipito.
Pakukwera kumzindako anapeza anthu aakazi alikutuluka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?