Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? Nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wake wamkazi alinkudza nazo nkhosa.
Genesis 29:7 - Buku Lopatulika Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yakobe adati, “Popeza kuti kukali masana, ndipo nthaŵi yokazilonga sinakwane, bwanji osati muzimwetse madzi, muzitengenso kukazidyetsa?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati, “Taonani, dzuwa likanalipo ndipo nthawi yosonkhanitsa nkhosa sinakwane. Bwanji osazimwetsa madzi nkhosazi.” |
Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? Nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wake wamkazi alinkudza nazo nkhosa.
Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa.