Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.
Genesis 29:5 - Buku Lopatulika Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wake wa Nahori? Nati, Timdziwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wake wa Nahori? Nati, Timdziwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yakobe adafunsanso kuti, “Kodi Labani mwana wa Nahori mumamdziŵa?” Iwowo adayankha kuti, “Ee, timamdziŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anawafunsanso kuti, “Kodi Labani, mdzukulu wa Nahori mukumudziwa?” Iwo anayankha, “Inde tikumudziwa?” |
Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.
Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori.
Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.
Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki.