Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 29:4 - Buku Lopatulika

Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? Nati, Ndife a ku Harani.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? Nati, Ndife a ku Harani.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yakobe adaŵafunsa abusawo kuti, “Kodi abale anga mukuchokera kuti?” Iwowo adayankha kuti, “Tikuchokera ku Harani.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yakobo anafunsa abusawo kuti, “Abale anga, mwachokera kuti?” Iwo anayankha, “Tachokera ku Harani.”

Onani mutuwo



Genesis 29:4
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko.


Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.


Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harani;


Ndipo Yakobo anachoka mu Beereseba, nanka ku Harani.


Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake.


Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye mu Mesopotamiya, asanayambe kukhala mu Harani;


Pamenepo anatuluka m'dziko la Akaldeya namanga mu Harani: ndipo, kuchokera kumeneko, atamwalira atate wake, Mulungu anamsuntha alowe m'dziko lino, m'mene mukhalamo tsopano;