Ndipo anayang'ana, taonani, chitsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu.
Genesis 29:3 - Buku Lopatulika Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nkhosa zonsezo zitasonkhana pamodzi kumeneko, abusa oŵeta nkhosazo ndiwo ankachotsa mwalawo pachitsimepo, kuti nkhosa zaozo zimwe. Zitatha kumwako, ankakunkhunizanso mwalawo kutseka pachitsimepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amati nkhosa zonse zikasonkhana, abusawo ankagudubuza mwalawo, kuwuchotsa ndi kumwetsa madzi nkhosazo. Kenaka ankawubwezera mwalawo pamalo pake, pakamwa pa chitsimepo. |
Ndipo anayang'ana, taonani, chitsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu.
Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa.
Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa; ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza.
Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'madera ake, mu Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.