Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale.
Genesis 29:12 - Buku Lopatulika Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbale wake wa atate wake, kuti ndiye mwana wake wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbale wake wa atate wake, kuti ndiye mwana wake wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adamuuza kuti, “Ine ndine mwana wa Rebeka, mlongo wa atate ako.” Pomwepo Rakele adathamanga kukauza atate ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yakobo anawuza Rakele kuti iye ndi mwana wa Rebeka, mlongo wa abambo a Rakele uja. Choncho Rakele anathamanga nakawuza abambo ake. |
Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale.
Ndipo Isaki anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wake wa Betuele Mwaramu, mlongo wake wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau.