ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Genesis 28:8 - Buku Lopatulika ndipo Esau anaona kuti ana aakazi a Kanani sanakondweretse Isaki atate wake: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo Esau anaona kuti ana akazi a Kanani sanakondweretsa Isaki atate wake: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Esau adadziŵa kuti bambo wake Isaki sankaŵakonda akazi a ku Kanani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndiye pamenepo Esau anazindikira kuti abambo ake Isake sankakondwera ndi akazi a ku Kanaani; |
ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?
Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani.
Koma chimenechi sichinakondweretse Samuele, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samuele anapemphera kwa Yehova.