ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.
Genesis 28:7 - Buku Lopatulika ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wake ndi amake, nanka ku Padanaramu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wake ndi amake, nanka ku Padanaramu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adamva kuti Yakobe wamvera bambo wake ndi mai wake, ndipo kuti wapita ku Mesopotamiya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yakobo anamvera abambo ake ndi amayi ake ndi kupita ku Padanaramu. |
ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.
Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harani;
Ndipo anaona Esau kuti Isaki anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko; ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani;
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.
Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.