Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Genesis 28:2 - Buku Lopatulika Tauka, nupite ku Padanaramu, kunyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana aakazi a Labani mlongo wake wa amai ako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tauka, nupite ku Padanaramu, kunyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana akazi a Labani mlongo wake wa amai ako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Konzeka, upite ku Mesopotamiya, kwao kwa Betuele, bambo wa mai wakoyu. Kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa mai wako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Panopo upite ku Padanaramu, ku nyumba kwa Betueli abambo a amayi akowa, kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa amayi akowa. |
Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.
Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino.
ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.
Ndipo Isaki anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wake wa Betuele Mwaramu, mlongo wake wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau.
ndipo ananka nazo zoweta zake zonse, ndi chuma chake chonse anachisonkhanitsa, zoweta zake anaziona mu Padanaramu, kuti anke kwa Isaki atate wake ku dziko la Kanani.
sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.
Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumzinda wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mzindapo.
Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anachokera mu Padanaramu, namdalitsa iye.
Amenewo ndi ana aamuna a Leya, amene anambalira Yakobo ku Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.
Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa.
Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israele kuchokera mu Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika.