Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 28:17 - Buku Lopatulika

Ndipo anaopa, nati, Poopsa pompano! Pompano ndipo pa nyumba ya Mulungu, si penai, pompano ndipo pa chipata cha kumwamba.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anaopa, nati, Poopsa pompano! Pompano ndipo pa nyumba ya Mulungu, si penai, pompano ndipo pa chipata cha kumwamba.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono adachita mantha, nanena kuti, “Hi, malo ano ndi oopsa! Zoonadi pano mpa nyumba ya Mulungu ndiponso khomo la kumwamba.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsono anachita mantha ndipo anati, “Malo ano ndi woopsa ndithu. Zoonadi pano ndi pa nyumba ya Mulungu ndi khomo la kumwamba.”

Onani mutuwo



Genesis 28:17
16 Mawu Ofanana  

Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pamutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamutu pake.


ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.


ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.


Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.


Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.


Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu.


Samalira phazi lako popita kunyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zilikuchimwa.


Ndipo pamene ophunzira anamva, anagwa nkhope zao pansi, naopa kwakukulu.


Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha aakulu.


Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa.


kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.


ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu;


Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?


Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,


Nati Manowa kwa mkazi wake, Tidzafa ndithu pakuti taona Mulungu.