Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko.
Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Betele nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m'dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;
Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye mu Mesopotamiya, asanayambe kukhala mu Harani;