Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.
Genesis 27:45 - Buku Lopatulika mpaka utamchokera mkwiyo mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mpaka wakuchokera mkwiyo wa mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa mpaka mtima wa mbale wako utatsika ndi kuiŵala zonse zimene wamchitazi. Pa nthaŵiyo, ine ndidzatuma munthu kudzakutenga. Nanga nditayirenji inu ana anga aŵiri pa tsiku limodzi?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono mkwiyo wa mʼbale wakoyo ukadzatsika ndi kuyiwala zonse wamuchitirazi, ndidzatuma munthu kuti adzakutenge. Nanga nditayirenji nonse awiri nthawi imodzi?” |
Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.
Ndipo Yakobo anati kwa atate wake, Ndine Esau mwana wanu wamkulu; ndachita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine.
Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende padzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m'nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.