Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.
Genesis 27:40 - Buku Lopatulika Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ntchito yako idzakhala yomenya nkhondo, ndipo udzakhala wotumikira mbale wako. Koma ukadzatha kudzimasula, udzachokeratu m'goli la ulamuliro wake.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Udzakhala ndi moyo podalira lupanga ndipo udzatumikira mʼbale wako. Koma idzafika nthawi pamene udzakhala mfulu udzachotsa goli lake mʼkhosi mwako.” |
Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.
Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.
Ndipo anaika maboma mu Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.
Wakanthadi Aedomu, koma mtima wako wakukweza; ulemekezeke, nukhale kwanu; udziutsiranji tsoka, ungagwe iwe ndi Yuda pamodzi nawe;
Anapha Aedomu mu Chigwa cha Mchere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, nautcha dzina lake Yokotele mpaka lero lino.
Chinkana anatero, Aedomu anapanduka kupulumuka m'dzanja la Yuda mpaka lero lino; nthawi yomweyo anapanduka Alibina kupulumuka m'dzanja lake; chifukwa adasiya Yehova Mulungu wa makolo ake.
Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.
Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere padziko lapansi; sindinadzere kuponya mtendere, koma lupanga.