Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
Genesis 27:39 - Buku Lopatulika Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye, Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi, pa mame a kumwamba akudzera komwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye, Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi, pa mame a kumwamba akudzera komwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Isaki, bambo wakeyo, adamuuza kuti, “Pa malo ako okhalapo sipadzakhala konse chonde, mvula siidzagwa pa minda yako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Isake abambo ake anamuyankha kuti, “Malo ako okhalapo sadzabala dzinthu, ndipo mvula sidzagwa pa minda yako. |
Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
Mulungu akupatse iwe mame a kumwamba, ndi zonenepa za dziko lapansi, ndi tirigu wambiri ndi vinyo.
Ndipo za Yosefe anati, Yehova adalitse dziko lake; ndi zinthu zofunikatu za m'mwamba, ndi mame, ndi madzi okhala pansipo;
Ndipo Israele akhala mokhazikika pa yekha; kasupe wa Yakobo; akhala m'dziko la tirigu ndi vinyo; inde thambo lake likukha mame.
Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito.