Ndipo anati Yakobo, Undilumbirire ine lero lomwe, ndipo analumbirira iye; nagulana ndi Yakobo ukulu wake.
Genesis 27:32 - Buku Lopatulika Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Ndiwe yani? Ndipo iye anati, Ndine mwana wanu woyamba Esau. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Ndiwe yani? Ndipo iye anati, Ndine mwana wanu woyamba Esau. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Isaki adamufunsa kuti, “Kodi iwenso ndiwe yani?” Iye adayankha kuti, “Ndine mwana wanu wamkulu Esau.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abambo ake, Isake, anamufunsa kuti, “Ndiwe yani?” Iye anayankha, “Ndine mwana wanu woyamba Esau.” |
Ndipo anati Yakobo, Undilumbirire ine lero lomwe, ndipo analumbirira iye; nagulana ndi Yakobo ukulu wake.
Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita: chomwecho Esau ananyoza ukulu wake.
Ndipo iye analowa kwa atate wake, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga?