Ndipo Isaki anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi chaka chimenecho; ndipo Yehova anamdalitsa iye.
Genesis 27:27 - Buku Lopatulika Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atabwera pafupi kudzampsompsona Isaki adanunkhiza zovala zimene Yakobe adaavala, ndipo pompo adamdalitsa, adati, “Fungo lokoma la mwana wanga lili ngati fungo la zokolola za m'munda umene Chauta adaudalitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anapita namupsompsona. Apa Isake anamva fungo la zovala zake, ndipo anamudalitsa nati, “Haa, fungo la mwana wanga lili ngati fungo la munda umene Yehova waudalitsa. |
Ndipo Isaki anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi chaka chimenecho; ndipo Yehova anamdalitsa iye.
Ndipo Rebeka anatenga zovala zokoma za Esau mwana wake wamkulu zinali m'nyumba, naveka nazo Yakobo mwana wake wamng'ono;
Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye, Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi, pa mame a kumwamba akudzera komwe.
Koma maso a Israele anali akhungu mu ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.
Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pake anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isaki, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero,
Mukhutitsa nthaka yake yolima; mufafaniza nthumbira zake; muiolowetsa ndi mvumbi; mudalitsa mmera wake.
Mkuyu utchetsa nkhuyu zake zosakhwima, mipesa niphuka, inunkhira bwino. Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.
Ndipo za Yosefe anati, Yehova adalitse dziko lake; ndi zinthu zofunikatu za m'mwamba, ndi mame, ndi madzi okhala pansipo;
Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawirikawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu: