Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye.
Genesis 27:26 - Buku Lopatulika Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono bambo wakeyo adati, “Bwera pafupi, udzandimpsompsone, mwana wanga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Isake anati kwa Yakobo, “Bwera kuno mwana wanga undipsompsone.” |
Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye.
Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
Chomwecho Yowabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yake pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu.