Genesis 27:25 - Buku Lopatulika Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Isaki adati, “Bwera nayo kuno nyama yako, kuti ndidye ndipo ndikudalitse.” Yakobe adabwera ndi nyamayo, Isaki nkudya. Yakobe adampatsanso vinyo woti amwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo iye anati, “Mwana wanga, patseko nyama yakoyo ndidye kuti ndikudalitse.” Yakobo anabwera ndi nyama ija kwa Isake ndipo anadya. Kenaka anamupatsanso vinyo ndipo anamwa. |
nundikonzere ine chakudya chokolera chonga chomwe ndichikonda ine, nudze nacho kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe.